Tizinyama totchedwa Koala tikutha chifukwa cha matenda opatsirana
Mu dziko la Australia, zinyama zotchdwa Koala, zimene zinali ndi chiwelengelo chambiri, zikutha. Izi zikuchitika chifukwa cha matenda opatsirana (STI) otchedwa Clamydia.
Clamydia ndi bacterial infection imene imavuta mwa anthu komanso zinyama. Clamydia amapatsirana poganana. Kwa anthu, makhwala ake ndi ma antibiotic.
zinyama zina zimapatsirananso matendawa koma kafukufuku akusonyeza kuti matendawa asanduka muliri umene ukuchepetsa chiwelengelo cha ma Koala. A katswiri ali pakalikiliki opanga vaccine kuti athandize zinyamazi.