Dziko la Zimbabwe lathetsa chilango cha imfa/kunyonga kwa akayidi awo
President wa dziko la Zimbabwe wavomereza lamulo latsopano lothedza chilango chonyonga kapena kupha akayidi.
Bungwe la Amnesty lati ndilokondwa ndi lamulo latsopanoli ngakhale anena kuti likhoza kusinthidwa nthawi iliyonse.
Akuti mkayidi otsiliza kuphedwa, ananyongedwa mu chaka cha 2005 ndipo sipananyongedwenso munthu ngakhale zigamulo zonyonga zakhala zikupelekedwa.
Kumapeto kwa chaka cha 2023, panali akayidi 60 amene anagamulidwa kuti aphedwe.
Akuti bwalo la milandu ichotsa chilango cha infa ndipo lipereka zilango zina.
Sidenote
Mwina bola choncho