Uganda - Ayamba kupereka vaccine wa nthenda ya Ebola

Mu dziko la Uganda, a chipatala ayamba kupereka vaccine wa matenda a Ebola.

Izi zabwera kutsatira imfa ya munthu mmodzi komanso kudwala kwa anthu awiri chifukwa cha matendawa.

Pali chikhulupiliro chakuti nthendayi yachoka ku Sudan ndipo ilibe vaccine (Sudan strain).

Nthenda ya ebola ilibe mankhwala, imafala msanga ndipo imapha mozunza.

Pali vaccine wa Zaire strain yemwe akufuna kuyeselera kuti mwina angathetse kufala kwa matendawa.

#nkhani

Previous
Previous

Sister Claire - Ulendo okhala Saint

Next
Next

Ndege yagwa ku South Sudan