Ndege yagwa ku South Sudan
Pa 29 January 2025, ndege imene inanyamula anthu 21 ogwira ntchito ku company ya mafuta, Greater Pioneer Operating company, inapanga ngozi. Ndegeyi inali itangonyamuka kumene ulendo opita ku mzinda wa Juba pamene inagwera pafupi ndi Unity oilfield airport ku South Sudan's Unity State.
Anthu 20 anafa ndipo munthu mmodzi wapulumuka, akulandira chithandizo ku chipatala.
Pali chikhulupiliro chakuti ndegeyi inanyamula katundu olemera kuposa muyeso, koma pakali pano, akufufuzabe chimene chapangitsa ngoziyi.