Imam waphedwa ku South Africa

Bambo uyu, Muhsin Hendricks, wa dzaka 57 waphedwa dzulo ku South Africa.

Muhsin anali Imam ku chipembedzo cha chisilamu ndipo mu chaka cha 1996, anawulula kuti iye anali gay.

Wakhala akupitiliza ntchito yake mu Mosque ndikulimbikitsa ma gay.

Dzulo waphedwa galimoto imene amayendera itapangidwa chifwamba.

Muhsin waphedwa atamaliza kudalitsa ukwati wa ma gay (lebsian) pamene ma Sheikh ena anakana.

Nde pali chikhulupiliro kuti waphedwa chifukwa cha zimenezo.

#thejakishow

Previous
Previous

Snow wa ku China

Next
Next

Mayi anaphedwa ndi Hippopotamus ku Zambia