Mayi anaphedwa ndi Hippopotamus ku Zambia
Bambo wina wa ku USA, Craig Manders, wasumila eni ake a safari, African portfolio pa imfa ya mkazi wake. Craig ndi mkazi wake Lisa, wa dzaka 70, anapita ku Zambia mu chaka cha 2024 kukaona zinyama za mthengo.
Anamagona ku Chiawa lodge. Pa 5 June 2024, Craig ndi Lisa anatengana ndi anthu ena, kuphatikiza ma guide ndi a security kupita kuyenda mnthengo. Akuti anafika pa mtsinje wina nkuyima pafupi atawonamo Hippopotamus. Gululi linayamba kujambula Hippopotamus yo.
Koma Hippo ija inangodzambatuka nkuyamba kuthamangira kunali anthuwo. Onse, kuphatikiza a security okuti anali ndi mfuti anathawa. Lisa anakanika kuthawa ndipo anagwidwa ndi Hippo.
Hippo inamuluma Lisa, kumupukusa, nkumuswa mutu. Lisa anafa mamuna wake ndi anthu ena akuwona.
Craig akusumira eni Safari chifukwa sanawateteze ndipo akufuna ndalama zokwana $15000.