Chigamulo chowawa

Mu chaka cha 2015, ku USA, bambo uyu Shane Ramsundar, wadzaka 52, pamodzi ndi mkazi wake, Gomatee, wa dzaka 48, ndi mwana wawo, Shantal, wadzaka 23, analandira dzigamulo zodabwitsa.

Atatuwa, amene kwawo kwenikweni kunali ku Trinidad, anayamba kupanga scam anthu powanamiza kuti awathandiza kuti akhazikike mu dziko la USA.

Anthuwa amawakhulupilira mpaka kumalipira ndalama zambiri.

Atatuwa, ankangodya ndalamazo. Anadya ndalama zokwana $1.8million.

Anagwidwa, kuzengedwa mulangu nkupezeka olakwa, analandira chigamulo ichi.

Shane Ramsundar, dzaka 235 mundende. Gomatee, dzaka 153 mundende. Mwana wawo Shantal, dzaka 30 mundende.

Pamodzi analandira chigamulo cha dzaka 418 mundende.

Previous
Previous

Mayi anaphedwa ndi Hippopotamus ku Zambia

Next
Next

2Baba Idibia wapeza mkazi wina