Katswiri wamangidwa
Ku USA, mayi uyu, Yvonne Woods, yemwe anali forensic scientist akuzengedwa mulandu.
Yvonne anali katswiri anali yemwe ma court amamudalira popereka ndi kuwunikira umboni wa DNA pa milandu ya criminal.
Pali chikhulupiliro chakuti Yvonne samapita ku lab kukafufuza kanthu, amangolemba malinga ndi mmene amafunira kuti mulandu uyendere.
Akuti pena amapereka umboni kuti wapeza DNA ya munthu ozengedwa mulandu zili zabodza.
Pena amajudula zithunzi za malo omwe papangikira chiwembu, kugwiritsa ntchito AI kuwonjezerapo magazi nkunama kuti magaziwo ndi a munthu oganizilidwayo.
Pena amanena kuti DNA yapezeka siyamunthu yemwe akuzengedwa mulandu mpaka munthu osamangidwa ali olakwa.
Amangopanga za opposite mpaka anthu pafupifupi 652 anamangidwa pogwiritsa ntchito umboni wa Yvonne, ngati katswiri.
Akatswiri ena akufufuza ntchito yakeyo. Yvonne wakhala akugwira ntchitoyi kwa dzaka 30.
Milandu yonse imene iye anapereka umboni ikupangidwa review.
Akapezeka olakwa, Yvonne akhoza kugamulidwa kuti akhale ku ndende kwa dzaka 40 kapena moyo wake onse.