Dingo wandidyera mwana
Pa 17 August 1980, mayi awa, Lindy Chamberlain, anatengana ndi amuna awo, ana awo ndi anzawo kupita ku camp ku camp m’dela la Uluru mu dziko la Australia.
Mwana wawo wamg’ono kwambiri anali Azaria, wa masabata 9 (9 weeks old).
Lindy anamutenga Azaiya nkumugoneka mu tent, kenako anapita panja pa tent kukacheza ndi anthu ena. Atabwelera kuti akamuone mwana, anapeza palibepo, anafuula anthu nkubwera. Amusaka mwana paliponse koma osamupeza. Anangopeza magazi malo angapo. Apolisi nawo anapita kukathandiza, anapeza baby suit ya Azaria ili ndi magazi.
Lindy ananenetsa kuti pamwamba pa baby suit, anamuveka Azaria coat, koma coat siinapezeke paliponse. A Polisi anayamba kumukayikira Lindy. Baby suit inapezekayo inali yong’ambika cha pakhosi, pamene panali magazi ambiri. Anapitista kwa ma expert ndipo ma expert anati zikusonyeza kuti Lindy anamucheka mwana wake pakhosi nkukamutaya ndipo nkhani yakuti panali coat yomwe mwana anavala inali yabodza chifukwa bwezi a Polisi atayipeza.
Lindy anapezeka olakwa pa mulanduwu, ngakhale iye ananenetsa kuti amakhulupilira kuti Dingo (galu wa mtchire) anamuba mwanaya. Lindy anapatsidwa chigamulo kuti akhale moyo wake onse ku prison ndipo anamutsekera chaka cha 1982.
Mu chaka che 1986, bambo wina, David Brett, anachoka kwawo ku Britain kupita kukayenda ku Australia. Anapita kukakwera miyala ya ku Uluru. Kumeneko, David Brett agagwa ndikufa.
Zinatenga masiku 8 kuti amupeze. Pamene anapeza thupi la David, anapezaponso ka Jacket ka mwana pafupi. Jacket inali ndendende, imene Lindy ankanena kuti anamuveka mwana wake ndipo inali ndi magazi. Malowa anali kutali kwambiri ndi kumune anasowa Azaria ndipo pafupi panali malo amene ma Dingo amasonkhana.
Lindy anatulutsidwa mundende chifukwa uwu unali umboni wakuti Azariya anabedwa nkudyedwa ndi Dingo.
Boma linamupepesa Lindy ndi ndalama zokwana $1.3 million.