Mayi olusa wamangidwa

Ku USA, Asisi awa, Latorray Collins, a dzaka 38, amangidwa.

Latorray anali okwiya chifukwa mamuna yemwe anali naye pa ubwenzi anathetsa chibwenzicho.

Latorray anakhala akumuyimbira phone mamunayo kuti akatenge katundu wake kunyumba kwake.

Mamunayo anamuuza Latorray kuti ataye katunduyo iye sakumufuna.

Mamunayo anali akupita ku date ndi bwenzi lanyuwani.

Ali pamsewu, anangodabwa galimoto ya Latorray ikuwalondola. Atayima pa traffic lights, Latorray anawatchingira, kutuluka mgalimoto, nkumuwombera mkazi winayo mmutu.

Latorray akudikira kukayankha mulandu ngakhale wanena kuti inali ngozi, anangophuluza pamene amafuna kuwombera m'wamba.

#Nkhani

Next
Next

Snow wa ku China